Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 2:3 - Buku Lopatulika

3 Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Zishango za ankhondo ao nzofiira, asilikali ao onse avala zovala zamlangali. Atandanda pa mizere yankhondo, magaleta ao akuchezimira ngati malaŵi a moto. Akavalo akungoti jodojodo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Zishango za ankhondo ake ndi zofiira; asilikali ake avala zovala zofiirira. Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira tsiku la kukonzekera kwake. Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 2:3
13 Mawu Ofanana  

Phodo likuti kochokocho panthiti pake, mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.


Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya.


Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebanoni, ndi kunena, Chigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.


Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Tiro Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, yochokera kumpoto ndi akavalo, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.


Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;


Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.


Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.


Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda;


Ndipo chinaoneka chizindikiro china m'mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri.


Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa