Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 2:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Patsala pang'ono kuti Chauta abwezere ulemerero wa Israele, monga udaaliri kale, ofunkha asanalande zinthu zonse ndi kuwononga mphesa zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo ngati ulemerero wa Israeli, ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu ndipo anawononganso mpesa wawo.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 2:2
14 Mawu Ofanana  

Atisankhira cholowa chathu, chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.


Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.


Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mzinda umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.


Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.


Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?


Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;


Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao zilizonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anachimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.


Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.


Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa