Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 9:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kungoti munthu saidziŵa nthaŵi yake. Monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, monga momwenso mbalame zimakodwera mu msampha, anthunso nchimodzimodzi. Amachita ngati kukodwa mu msampha pa nthaŵi yoipa, pamene tsoka laŵagwera mwadzidzidzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti: monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha, chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa, pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 9:12
28 Mawu Ofanana  

Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka; ndipo ndani adziwa chionongeko cha zaka zao?


M'kulakwa kwa woipa muli msampha; koma wolungama aimba, nakondwera.


Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.


Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.


Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.


Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.


Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu;


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga.


Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.


Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake.


Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.


(pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa