Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 8:14 - Buku Lopatulika

14 Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:14
16 Mawu Ofanana  

Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa.


Oipa akhaliranji ndi moyo, nakalamba, nalemera kwakukulu?


Taonani, inu nonse munachiona; ndipo mugwidwa nazo zopanda pake chifukwa ninji?


Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.


Pali choipa ndachiona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkulu;


Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa