Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 5:14 - Buku Lopatulika

14 koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lake mulibe kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lake mulibe kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka, kotero kuti pamene wabereka mwana alibe kanthu koti amusiyire.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 5:14
17 Mawu Ofanana  

nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni.


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo, ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;


Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.


Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake.


Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa