Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 3:20 - Buku Lopatulika

20 Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 3:20
20 Mawu Ofanana  

Zaka za moyo wa Ismaele ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake.


Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Koma munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?


Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.


Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga; ndikayala pogona panga mumdima.


Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi? Akati aonongeke, safuulako kodi?


zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi, ndi munthu adzabwerera kufumbi.


Mtambo wapita watha, momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.


Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.


Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.


Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa.


fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.


Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?


akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?


Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.


Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa