Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 2:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Tsono ndani amadziŵa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala womalamulira zonse zimene ndidazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Zimenezinso nzopanda phindu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:19
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.


M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?


Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu;


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa