Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 10:14 - Buku Lopatulika

14 Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chitsiru chimangochulutsa mau. Kodi ndani angadziŵe zimene zidzachitike kutsogolo? Ndani angathe kumuuza munthu zimene zidzachitike iye atafa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu. Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo, ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:14
13 Mawu Ofanana  

Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu, asansa manja pakati pa ife, nachulukitsa maneno ake pa Mulungu.


chifukwa chake Yobu anatsegula pakamwa pake mwachabe, nachulukitsa mau opanda nzeru.


Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.


Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.


Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumzinda.


M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?


Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.


pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa?


Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao.


Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa