Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 4:2 - Buku Lopatulika

2 pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino. Choncho musasiye malangizo anga.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 4:2
15 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira;


Pakuti unena, Chiphunzitso changa nchoona, ndipo ndili woyera pamaso pako.


Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.


Akadandithera padziko lapansi; koma ine sindinasiye malangizo anu.


Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;


Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu aamuna ndi aakazi;


Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.


Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa