Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 2:4 - Buku Lopatulika

4 ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 2:4
20 Mawu Ofanana  

Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.


wakuyembekezera imfa, koma kuli zii, ndi kuikumba koposa chuma chobisika,


Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka.


Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.


Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi.


Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.


Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?


ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire;


Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.


Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.


Akundikonda ndiwakonda; akundifunafuna adzandipeza.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.


Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa