Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 2:2 - Buku Lopatulika

2 kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 2:2
15 Mawu Ofanana  

Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru.


Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.


ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire;


Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mau anzeru.


Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha;


Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga.


Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;


Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Amene ali ndi makutu, amve.


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa