Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 13:2 - Buku Lopatulika

2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Munthu wabwino amapeza nako phindu kulankhula kwake, koma anthu onyenga amalakalaka zandeu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake, koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 13:2
16 Mawu Ofanana  

Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.


Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.


ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao.


momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.


Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha; koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.


Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.


Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwake; iye nadzakhuta phindu la milomo yake.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba.


Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu.


Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa