Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 11:10 - Buku Lopatulika

10 Olungama akapeza bwino, mzinda usekera; nufuula pakuonongeka oipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Olungama akapeza bwino, mudzi usekera; nufuula pakuonongeka oipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mulungu akamadalitsa anthu ake, mzinda wonse umatukuka. Oipa akaonongeka, anthu amafuula mwachimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera, ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 11:10
14 Mawu Ofanana  

Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mzinda munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu.


napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.


Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mzinda munali chete, atamupha Ataliya ndi lupanga.


Anthu adzamuombera manja, nadzamuimbira mluzu achoke m'malo mwake.


Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.


Madalitso a olungama akuza mzinda; koma m'kamwa mwa oipa muupasula.


Posekera olungama pali ulemerero wambiri; koma pouka oipa anthu amabisala.


Pouka oipa anthu amabisala; koma pakufa amenewo olungama achuluka.


Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.


Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m'menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa