Mateyu 27:64 - Buku Lopatulika64 Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201464 Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa64 Tsono mulamule kuti azilondapo pamanda pake mpaka mkucha. Tikuwopa kuti ophunzira ake angadzabwere nkudzaba mtembo wake, kenaka namadzauza anthu kuti ‘Iye uja wauka kwa akufa.’ Apo kunyenga kotsirizaku kudzakhala koipa zedi kupambana koyamba kuja.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero64 Choncho lamulirani kuti manda ake atetezedwe mpaka pa tsiku lachitatu. Chifukwa tikapanda kutero, ophunzira ake angabwere kudzaba mtembo wake ndipo angawuze anthu kuti waukitsidwa kwa akufa. Ndipo chinyengo chomalizachi chidzakhala choyipa kwambiri kusiyana ndi choyamba chija.” Onani mutuwo |