Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 25:44 - Buku Lopatulika

44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife osachitapo kanthu?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:44
14 Mawu Ofanana  

Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;


Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwe.


Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?


Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani?


Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama.


ndinali mlendo, ndipo simunandilandire Ine; wamaliseche ndipo simunandiveke Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadze kundiona Ine.


Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.


Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.


Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa