Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 25:43 - Buku Lopatulika

43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandire Ine; wamaliseche ndipo simunandiveke Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadze kundiona Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamaliseche ndipo simunandiveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Ndidaali mlendo, inu osandilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu osandiveka. Ndinkadwala, ndidaalinso m'ndende, inu osadzandichetsa.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:43
10 Mawu Ofanana  

Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala, kapena kuti wosowa alibe chofunda;


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonde; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova.


Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa.


wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.


pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatse Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetse Ine:


Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.


Napatukirako, kuti alowe nagone ku Gibea; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mzindawo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa