Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 25:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:20
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.


Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.


Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa