Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 25:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 25:14
13 Mawu Ofanana  

Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.


Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.


Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo.


Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa