Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 23:39 - Buku Lopatulika

39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Chifukwa chake ndikuwuza kuti simudzandionanso kufikira pamene mudzati, ‘Wodala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:39
15 Mawu Ofanana  

Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova; takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona.


Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.


Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.


Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona nasangalala.


Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa