Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 23:35 - Buku Lopatulika

35 kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Motero chilango chidzakugwerani chifukwa cha anthu olungama onse amene adaphedwa, kuyambira kuphedwa kwa Abele, munthu wolungama uja, mpaka kuphedwa kwa Zakariya, mwana wa Barakiya, amene mudamuphera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa lansembe ndi Malo Opatulika kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:35
22 Mawu Ofanana  

Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.


Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.


ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.


Konzani inu popherapo ana ake, chifukwa cha kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzuka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi mizinda.


Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.


Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.


ndipo anamtulutsa Uriya mu Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa