Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 23:16 - Buku Lopatulika

16 Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:16
14 Mawu Ofanana  

Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?


Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?


Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira.


Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.


Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.


Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa