Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:15 - Buku Lopatulika

15 Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaona zodabwitsa zimene Iye ankachita. Adamvanso ana akufuula m'Nyumba ya Mulungu kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide.” Ndiye iwowo adapsa nazo mtima,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:15
20 Mawu Ofanana  

Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.


Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu.


Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.


Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu mu Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.


Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,


Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane


Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa