Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 18:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa mu Gehena wamoto, uli ndi maso awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m'Gehena wamoto, uli ndi maso awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 18:9
11 Mawu Ofanana  

Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.


Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena.


Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu Gehena;


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa