Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 89:8 - Buku Lopatulika

8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova? Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova? Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu? Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 89:8
19 Mawu Ofanana  

ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;


Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira, Mulungu ali nao ukulu woopsa.


Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu? Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?


Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha.


Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zazikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Muli nao mkono wanu wolimba; m'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.


Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?


Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.


Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu, oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.


Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.


Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,


Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?


Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa