Masalimo 89:41 - Buku Lopatulika41 Onse opita panjirapa amfunkhira, akhala chotonza cha anansi ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Onse opita panjirapa amfunkhira, akhala chotonza cha anansi ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Onse odutsa amamlanda zinthu zake, anzake amamunyodola. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake; iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake. Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.