Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 88:5 - Buku Lopatulika

5 Wotayika pakati pa akufa, ngati ophedwa akugona m'manda, amene simuwakumbukiranso; ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Wotayika pakati pa akufa, ngati ophedwa akugona m'manda, amene simuwakumbukiranso; ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndili ngati munthu womsiya yekha pakati pa anthu akufa, ngati munthu wophedwa amene wagona m'manda. Ndili ngati anthu amene Inu simuŵakumbukiranso, popeza kuti ndi ochotsedwa m'manja mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 88:5
15 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Mulungu anaononga mizinda ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga mizinda m'mene anakhalamo Loti.


Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;


Akapita, nakatsekera, nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?


Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika, kumanda kwandikonzekeratu.


Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!


Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.


Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.


Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka.


Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


Kuzaza kwanu kwandimiza; zoopsa zanu zinandiononga.


Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa