Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 88:12 - Buku Lopatulika

12 Zodabwitsa zanu zidzadziwika mumdima kodi, ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Zodabwitsa zanu zidadziwika mumdima kodi, ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kodi zodabwitsa zanu zimadziŵika mu mdima? Ndani angadziŵe za chithandizo chanu chopulumutsa m'dziko la anthu oiŵalika?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima, kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 88:12
10 Mawu Ofanana  

Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.


Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka.


Wotayika pakati pa akufa, ngati ophedwa akugona m'manda, amene simuwakumbukiranso; ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.


Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.


Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.


Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.


nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.


koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.


mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa