Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 88:11 - Buku Lopatulika

11 Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Kodi chikondi chanu chosasinthikacho amachilalikira ku manda? Kodi amasimba za kukhulupirika kwanu ku malo achiwonongeko?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda, za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 88:11
11 Mawu Ofanana  

Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka? Natulutsidwa tsiku la mkwiyo?


Kumanda kuli padagu pamaso pake, ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.


Indedi muwaika poterera, muwagwetsa kuti muwaononge.


Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.


Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.


Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?


Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa