Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 86:14 - Buku Lopatulika

14 Mulungu, odzikuza andiukira, ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga, ndipo sanaike Inu pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Mulungu, odzikuza andiukira, ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga, ndipo sanaike Inu pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Inu Mulungu, anthu achipongwe andiwukira. Anthu opanda chifundo akufunafuna moyo wanga ndipo sasamala za Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufuna kundipha, amene salabadira za Inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 86:14
21 Mawu Ofanana  

Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.


Woipa anyozeranji Mulungu, anena m'mtima mwake, Simudzafunsira?


Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.


Odzikuza anandinyoza kwambiri: koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.


Odzikuza anandipangira bodza: Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.


Odzikuza anandikumbira mbuna, ndiwo osasamalira chilamulo chanu.


Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.


Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse.


Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.


Adzabwezera choipa adani anga, aduleni m'choonadi chanu.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.


Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa