Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:49 - Buku Lopatulika

49 Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo: adaŵapsera mtima naŵakwiyira nkuŵagwetsera mavuto. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:49
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi.


Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.


Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.


Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.


Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake; anayatsa moto mu Ziyoni, unanyambita maziko ake.


Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa