Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:43 - Buku Lopatulika

43 Amene anaika zizindikiro zake mu Ejipito, ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Amene anaika zizindikiro zake m'Ejipito, ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 pamene Iye adachita zizindikiro zamphamvu ku Ejipito, ndiponso zozizwitsa zake ku dera la ku Zowani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto, zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:43
10 Mawu Ofanana  

nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.


Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.


Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m'dziko la Ejipito.


Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa mu Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa