Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:26 - Buku Lopatulika

26 Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Adakunthitsa mphepo yakuvuma mu mlengalenga, adatulutsa mphepo yakumwera ndi mphamvu zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba, ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:26
5 Mawu Ofanana  

Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.


Atumiza mau ake nazisungunula; aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.


Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.


Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, n'kudza nazo zinziri zochokera kunyanja, ndipo zidagwa kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.


Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa