Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:15 - Buku Lopatulika

15 Anang'alula thanthwe m'chipululu, ndipo anawamwetsa kochuluka monga m'madzi ozama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Anang'alula thanthwe m'chipululu, ndipo anawamwetsa kochuluka monga m'madzi ozama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Adang'amba matanthwe am'chipululu, naŵapatsa madzi ochuluka ngati amumtsinje, kuti amwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:15
11 Mawu Ofanana  

Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi; nayenda pouma ngati mtsinje.


amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.


Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe mu Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.


Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.


Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;


Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.


Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.


namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.


Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa