Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:32 - Buku Lopatulika

32 Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu; imbirani Ambuye zomlemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu; imbirani Ambuye zomlemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Imbirani Mulungu nyimbo, inu maufumu a pa dziko lapansi. Imbani nyimbo zotamanda Ambuye,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi imbirani Ambuye matamando. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:32
9 Mawu Ofanana  

Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.


Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu, ndi maufumu kuti atumikire Yehova.


Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.


Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.


Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa