Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:23 - Buku Lopatulika

23 kuti uviike phazi lako m'mwazi, kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 kuti uviike phazi lako m'mwazi, kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 kuti musambe mapazi anu m'magazi, kuti agalu anu anyambiteko magazi a adaniwo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu, pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:23
7 Mawu Ofanana  

Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.


Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.


Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.


Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa