Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:14 - Buku Lopatulika

14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala mu Zalimoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala m'Zalimoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko, zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:14
10 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.


Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoyamba za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.


Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.


Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.


Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa