Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 58:9 - Buku Lopatulika

9 Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Miphika yanu isanagwire moto wa nkhuni zaminga, zingakhale zaziŵisi kapena zoyaka, Mulungu aziseseretu nkuzichotsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku, kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:9
17 Mawu Ofanana  

Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima; adzampirikitsa achoke m'dziko lokhalamo anthu.


Mphepo ya kum'mawa imtenga, nachoka iye; nimkankha achoke m'malo mwake.


Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zii; ngati makanda osaona kuunika.


Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.


Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola.


Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula, ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu; pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.


Monga kavumvulu angopita, momwemo woipa kuli zii; koma olungama ndiwo maziko osatha.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.


Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.


Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.


Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.


Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa