Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 55:19 - Buku Lopatulika

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mulungu, amene akukhala pa mpando waufumu kuyambira kalekale, adzandimenyera nkhondo, adzaŵatsitsa adani anga chifukwa safuna kusintha khalidwe lao loipa, ndipo saopa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya, adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga, chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa ndipo saopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 55:19
15 Mawu Ofanana  

Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.


Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.


Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele;


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.


Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?


Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthike.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.


Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.


Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa