Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 55:13 - Buku Lopatulika

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 55:13
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.


Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.


Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse, kuti ndiwabwezere.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine.


Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa