Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 50:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti zamoyo zonse zakuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 50:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.


Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.


Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.


Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;


Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.


ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa