Masalimo 49:13 - Buku Lopatulika13 Njira yao ino ndiyo kupusa kwao, koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Njira yao yino ndiyo kupusa kwao, koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Zimenezi ndizo zimene zimaŵagwera anthu amene ali ndi chikhulupiriro chopusa, ndiwo mathero ake a onse amene amatsata maganizo otere. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. Sela Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.