Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 46:8 - Buku Lopatulika

8 Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Bwerani kuti muwone ntchito za Chauta, m'mene amachitira zozizwitsa pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 46:8
18 Mawu Ofanana  

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.


Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira, adzandionetsa tsoka la adani anga.


Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.


Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?


Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu mu Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo.


Taonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ake.


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.


Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.


Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ali ndi inu.


Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa