Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 44:18 - Buku Lopatulika

18 Mtima wathu sunabwerere m'mbuyo, ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuke m'njira yanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo, ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Mtima wathu sudabwerere m'mbuyo, mapazi athu sadaleke kuyenda m'njira yanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo; mapazi athu sanatayike pa njira yanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 44:18
12 Mawu Ofanana  

chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.


popeza anapatuka, naleka kumtsata, osasamalira njira zake zilizonse.


Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukane nazo mboni zanu.


Odzikuza anandinyoza kwambiri: koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.


Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.


koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda.


Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.


ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.


Kumbukirani mkazi wa Loti.


Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa