Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:18 - Buku Lopatulika

18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo chosiyira chao chidzakhala chosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova, ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:18
22 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.


Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.


Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu, pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.


Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.


Ndidzaoperanji masiku oipa, pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?


Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.


Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko, angwiro nadzatsalamo.


Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.


Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.


kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.


Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa; ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa