Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 35:3 - Buku Lopatulika

3 Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola. Nenani ndi moyo wanga, Chipulumutso chako ndine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola. Nenani ndi moyo wanga, Chipulumutso chako ndine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tengani mkondo ndi nthungo, kuti mulimbane nawo anthu ondilondola. Uzani mtima wanga kuti, “Mpulumutsi wako ndine.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tengani mkondo ndi nthungo, kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa. Uzani moyo wanga kuti, “Ine ndine chipulumutso chako.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 35:3
13 Mawu Ofanana  

Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.


Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.


Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.


Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.


Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.


Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu,


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa