Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 31:11 - Buku Lopatulika

11 Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adani anga onse amandinyodola, anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa. Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa. Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Chifukwa cha adani anga onse, ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga; ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga. Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 31:11
24 Mawu Ofanana  

Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.


Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali.


Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa.


Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima.


Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.


Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake.


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.


Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.


Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.


Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.


kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;


Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake.


Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa