Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:31 - Buku Lopatulika

31 Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu amene mpaka tsopano sanabadwe, ponena kuti Chauta ndiye adapulumutsa anthu ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake kwa anthu amene pano sanabadwe pakuti Iye wachita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:31
15 Mawu Ofanana  

Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.


Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.


kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.


Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.


Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.


Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa