Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 18:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Inu mwanditchinjiriza ndi chishango chanu chachipulumutso. Dzanja lanu lamanja landichirikiza, mwandikweza ndi chithandizo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Inu mumandipatsa chishango chachipambano, ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza; mumawerama pansi kundikuza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:35
12 Mawu Ofanana  

Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.


Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:


Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.


Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.


Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.


Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patali.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa