Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 145:13 - Buku Lopatulika

13 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 145:13
13 Mawu Ofanana  

Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya; aonongeka amitundu m'dziko lake.


Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Inu, Yehova, mukhala chikhalire, ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo.


Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.


Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.


Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.


Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.


pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa