Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:99 - Buku Lopatulika

99 Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

99 Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

99 Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse popeza ndimalingalira umboni wanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:99
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.


Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu.


Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa, ndizo zondipangira nzeru.


Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.


Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa